6. Pamene sanawapeza anakokera Yasoni ndi abale ena pamaso pa akuru a mudzi, napfuula kuti, Omwe aja asanduliza dziko lokhalamo anthu, afika kunonso;
7. amene Yasoni walandira; ndipo onsewo acita zokana malamulo a Kaisara; nanena kuti pali mfumu yina, Yesu.
8. Ndipo anabvuta anthu, ndi akuru a mudzi, pamene anamva zimenezi.
9. Ndipo pamene analandira cikole kwa Yasoni ndi enawo, anawamasula.
10. Pomwepo abale anatumiza Paulo ndi Sila usiku kunka ku Bereya; pamene iwo anafika komweko analowa m'sunagoge wa Ayuda.
11. Amenewa anali mfulu koposa a m'Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m'malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.
12. Ndipo ambiri a iwo anakhulupira; ndi akazi a Cihelene omveka, ndi amuna, osati owerengeka.
13. Koma pamene Ayuda a ku Tesalonika anazindikira kuti mau a Mulungu analalikidwa ndi Paulo ku Bereyanso, anadza komwekonso, nautsa, nabvuta makamu.
14. Pomwepo abale anaturutsa Paulo amuke kufikira kunyanja; koma Sila ndi Timoteo anakhalabe komweko.
15. Koma iwo amene anaperekeza Paulo anadza naye kufikira ku Atene; ndipo polandira iwo lamulo la kwa Sila ndi Timoteo kuti afulumire kudza kwa iye ndi cangu conse, anacoka.
16. Pamene Paulo analindira iwo pa Atene, anabvutidwa mtima pamene anaona mudzi wonse wadzala ndi mafano.
17. Cotero tsono anatsutsana ndi Ayuda ndi akupembedza m'sunagoge, ndi m'bwalo la malonda masiku onse ndi iwo amene anakomana nao.