Luka 18:8-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndinena ndi inu, adzawacitira cilungamo posacedwa. Koma Mwana wa munthu pakudza Iye, vadzapeza cikhulupiriro pa dziko lapansi kodi?

9. Ndipo anatinso kwa ena amene anadzikhulupirira mwa iwo okha kuti ali olungama, napeputsa onse ena, fanizo ili,

10. Anthu awiri anakwera kunka kukacisi kukapemphera; winayo Mfarisi ndi mnzace wamsonkho.

11. Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindiri monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, acigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu;

12. ndisala cakudya kawiri sabata limodzi; ndipereka limodzi lamagawo khumi la zonse ndiri nazo.

13. Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafuna kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pacifuwa pace nanena, Mulungu, mundicitire cifundo, ine wocimwa.

Luka 18