11. Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindiri monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, acigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu;
12. ndisala cakudya kawiri sabata limodzi; ndipereka limodzi lamagawo khumi la zonse ndiri nazo.
13. Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafuna kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pacifuwa pace nanena, Mulungu, mundicitire cifundo, ine wocimwa.