Levitiko 27:18-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Akaupatula munda wace citapita caka coliza lipenga, wansembe azimwerengera ndalama monga mwa zaka zotsalira kufikira caka coliza lipenga, nazicepsako pa kuyesa kwako.

19. Ndipo wakupacula mundayo akauomboladi, aonjezeko limodzi la magawo asanu la ndalama za kuyesa kwako, ndipo uzikhalitsa wace.

20. Koma akapanda kuombola mundawo, kapena atagulitsa mundawo kwa munthu wina, suomboledwanso;

Levitiko 27