4. Munthu ali yense wa mbeu za Aroni wokhala ndi khate, kapena kukha, asadyeko zinthu zopatulika, kufikira atayera. Ndipo ali yense wokhudza cinthu codetsedwa ndi wakufa, kapena mwamuna wogona uipa;
5. ndi ali yense wokhudza cinthu cokwawa cakudetsedwa naco, kapenanso munthu amene akamdetsa naco, codetsa cace ciri conse;
6. munthu wokhudza ciri conse cotere adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo, ndipo asadye zinthu zopatulika, akapanda kusamba thupi lace ndi madzi.
7. Koma litalowa dzuwa, adzakhala woyera, ndi pambuyo pace adyeko zoyerazo, popeza ndizo cakudya cace.
8. Asamadya zakufa zokha, kapena zojiwa, kudzidetsa nazo; Ine ndine Yehova.
9. Potero asunge cilangizo canga, angasenzepo ucimo, ndi kufera m'mwemo, pakuciipsa; Ine ndine Yehova wakuwapatula iwo,
10. Mlendo asadyeko copatulikaco; wakungokhala, ndi wansembe, kapena wolembedwa nchito, asadyeko copatulikaco.
11. Koma wansembe atakagula munthu ndi ndarama zace, iyeyu adyeko; ndi iwo amene anabadwa m'nyumba yace, adyeko mkate wace.