Hoseya 4:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo udzakhumudwa usana, ndi mneneri yemwe adzakhumudwa pamodzi ndi iwe usiku; ndipo ndidzaononga mai wako.

6. Anthu anga aonongeka cifukwa ca kusadziwa; popeza unakana kudziwa, Inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga; popeza waiwala cilamulo ca Mulungu wako, Inenso ndidzaiwala ana ako.

7. Monga anacuruka, momwemo anandicimwira; ndidzasanduliza ulemerero wao ukhale manyazi.

8. Adyerera cimo la anthu anga, nakhumbira cosalungama cao, yense ndi mtima wace.

9. Ndipo kudzakhala monga anthu, momwemo wansembe; ndipo ndidzawalanga cifukwa canjira zao, ndi kuwabwezera macitidwe ao.

Hoseya 4