11. Ndipo dziko lapansi linabvunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi ciwawa.
12. Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linabvunda; pakuti anthu onse anabvunditsa njira yao pa dziko lapansi.
13. Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Cimariziro cace ca anthu onse cafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi ciwawa cifukwa ca iwo; taonani, ndidzaononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi.
14. Udzipangire wekha cingalawa ca mtengo wanjale; upangemo zipinda m'cingalawamo, ndipo upake ndi utoto m'kati ndi kunja.
15. Kupanga kwace ndi kotere: m'litari mwace mwa cingalawa mikono mazana atatu, m'mimba mwace mikono makumi asanu, m'msinkhu mwace mikono makumi atatu.
16. Uike zenera m'ciogalawaco, ulimarize ndi kusiya mkono umodzi pamwamba pace: khomo la cingalawa uike m'mbali mwace; nucipange ndi nyumba yapansi, ndi yaciwiri, ndi yacitatu.