Genesis 49:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Simeoni ndi Levi ndiwo abale;Zida za mphulupulu ndizo malupanga ao.

6. Mtima wangawe, usalowe mu ciungwe cao;Ulemerero wanga, usadziphatike pa masonkhano ao;Cifukwa m'kukwiya kwao anapha munthu,M'kufuna kwao anapundula ng'ombe.

7. Kutembereredwekukwiyakwao, cifukwa kunali koopsya;Ndi kupsya mtima kwao, cifukwa kunali kwankharwe;Ndidzawagawanitsa m'YakoboNdidzabalalitsa iwo m'Israyeli.

8. Yuda, abale ako adzakuyamika iwe;Dzanja lako lidzakhala pa khosi la adani ako;Ana amuna a atate wako adzakuweramira.

9. Yuda ndi mwana wa mkango,Kucokera kuzomotola, mwananga, wakwera;Anawerama pansi, anabwatama ngati mkango,Ndipo ngati mkango waukazi; ndani adzamukitsa iye?

10. Ndodo yacifumu siidzacoka mwa Yuda,Kapena wolamulira pakati pa mapazi ace,Kufikira atadza Silo;Ndipo anthu adzamvera iye.

11. Adamanga mwana wa kavalo wace pampesa,Ndi mwana wa buru wace pa mpesa wosankhika;Natsuka malaya ace m'vinyo,Ndi copfunda cace m'mwazi wa mphesa.

Genesis 49