Genesis 44:16-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndico Yuda anati, Kodi tidzati bwanji kwa mbuyanga? kodi tidzanenanji? kapena tidzawiringula ife bwanji? Mulungu wapeza mphulupulu ya akapolo anu; taonani, tiri akapolo a mbuyanga, ife ndi iye amene anampeza naco cikho m'dzanja lace.

17. Ndipo iye anati, Ngati kutheka kuti ndicite cotero! Munthu amene anampeza naco m'dzanja lace adzakhala kapolo wanga: koma inu, kazipitani ndi mtendere kwa atate wanu.

18. Ndipo Yuda anayandikira kwa iye nati, Mfumu, kapolo wanu aneneretu m'makutu a mbuyanga, mtima wanu usapse pokwiya ndi kapolo wanu; cifukwa muli ngati Farao.

19. Mbuyanga anafunsa akapolo ace kuti, Kodi muli ndi atate wanu kapena mbale wanu?

Genesis 44