24. Ngati Kaini adzabwezeredwa kasanu ndi kawiri,Koma Lameke makumi asanu ndi awiri.
25. Ndipo Adamu anadziwanso mkazi wace; ndipo anabala mwana wamwamuna, namucha dzina lace Seti: Cifukwa, nati iye, Mulungu wandilowezera ine mbeu yina m'malo mwa Abele amene Kaini anamupha,
26. Ndiponso kwa Seti, kwa iye kunabadwamwana wamwamuna: anamucha dzina lace Enosi: pomwepo anthu anayamba kuchula dzina la Yehova.