15. Amenewa ndi mafumu a ana amuna a Esau: ana amuna a Elifazi woyamba wa Esau: mfumu Temani, mfumu Omari, mfumu Zefo, mfumu Kenazi,
16. mfumu Kora, mfumu Gatamu, mfumu Amaleki: amenewa ndi mafumu a kwa Elifazi m'dziko la Edomu: amenewa ndi ana amuna a Ada.
17. Amenewa ndi ana amuna a Reueli mwana wamwamuna wa Esau: mfumu Nahati, mfumu Zera, mfumu Sama, mfumu Miza; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Reueli m'dziko la Edomu: amenewa ndi ana amuna a Basemati mkazi wace wa Esau.
18. Amenewa ndi ana amuna a Oholibama mkazi wace wa Esau; mfumu Jeusi, mfumu Jalamu, mfumu Kora, amenewa ndi mafumu obadwa kwa Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mkazi wace wa Esau.