7. Ndipo mthenga wa Yehova anampeza iye pa kasupe wa madzi m'cipululu, pa kasupe wa pa njira ya ku Suri.
8. Ndipo anati, Hagara, mdzakazi wace wa Sarai, ufumira kuti? Unka kuti? Ndipo anati, Ndithawa ine kumaso kwace kwa wakuka wanga Sarai.
9. Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Bwera kwa wakuka wako, udzicepetse wekha pamanja pace.
10. Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ndidzacurukitsa ndithu mbeu zako, kuti unyinji wao sudzawerengeka.
11. Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Taona, uli ndi pakati, ndipo udzabala mwana wamwamuna; nudzamucha dzina lace Ismayeli; cifukwa Yehova anamva kusauka kwako.