Ezekieli 46:21-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Pamenepo anaturukira nane ku bwalo lakunja, nandipititsa ku ngondya zinai za bwaloli; ndipo taonani, m'ngondya monse munali bwalo.

22. M'ngondya zinai za bwalo munali mabwalo ocingika, m'litali mwace mikono makumi anai, kupingasa kwace makumi atatu; awa anai m'ngondyazi analingana muyeso wace.

23. Ndipo panali maguwa pozungulira pace m'menemo, pozungulira pace pa mabwalo anai; ndipo anamanga maguwawo ndi mafuwa pansi pace pozungulirapo.

24. Ndipo anati kwa ine, Izi ndi nyumba zophikiramo, kumene atumiki a kacisi aziphikira nsembe ya anthu.

Ezekieli 46