Ezekieli 41:16-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. ziundo, ndi mazenera a made okhazikika, ndi makonde am'mwamba akuzinga zipinda zosanjikizana zao zitatu, pandunji pa ciundo, ocinga ndi matabwa pozungulira pace, kuyambira pansi kufikira kumazenera; koma mazenera anaphimbika;

17. kufikira pamwamba pa khomo, mpaka nyumba ya m'katimo, ndi kunja kwace, ndi khoma lonse kwete m'kati ndi kunja, monga mwa miyeso.

18. Ndipo panalembedwapo ndi akerubi ndi akanjedza, kanjedza pakati pa akerubi; ndi kerubi ali yense anali ndi nkhope zace ziwiri;

19. nkhope ya munthu kuloza kukanjedza cakuno, ndi nkhope ya mwana wa mkango kuloza kukanjedza cauko, momwemo m'nyumba monse pozungulira pace.

20. Kuyambira pansi kufikira pamwamba pa khomo panalembedwa akerubi ndi akanjedza; linatero khoma la Kacisi.

21. Mphuthu za Kacisi zinali zamphwamphwa, ndi maonekedwe a pakhomo pa malo opatulika ananga maonekedwe a kacisi.

22. Guwa la nsembe linali lamtengo, msinkhu wace mikono itatu, ndi m'litali mwace mikono iwiri, ndi ngondya zace, ndi tsinde lace, ndi: thupi, nza mtengo; ndipo ananena ndi ine, Ili ndiko gome liri pamaso pa Yehova.

23. Ndipo Kacisi ndi malo opatulikitsa anali nazo zitseko ziwiri.

24. Ndipo pamakomopo panali zitseko zopatukana zotembenuzika, cina copatukana pa khomo lina cina pa linzace.

25. Ndipo panalembedwa pamenepo pa Izitseko za Kacisi akerubi ndi akanjedza, akunga aja adalembedwa pamakhoma; ndipo panali matabwa ocindikira pakhomo pakhonde panja,

26. Ndipo panali mazenera a made okhazikika, ndi akanjedza cakuno ndi cauko, kumbali zace za khonde; momwemonso pa zipinda za m'mphepete mwa nyumba, ndi pa matabwa ocindikira.

Ezekieli 41