Ezekieli 39:9-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo iwo okhala m'midzi ya Israyeli adzaturuka, nadzasonkha moto, nadzatentha zida za nkhondo, ndi zikopa zocinjiriza, mauta, ndi mibvi, ndi ndodo, ndi mikondo; ndipo adzasonkha moto nazo zaka zisanu ndi ziwiri;

10. osatenga nkhuni kuthengo, kapena kuzitema kunkhalango; popeza adzasonkha moto ndi zidazo; nadzafunkha iwo amene anawafunkha, ndi kulanda zao za iwo adalanda zaozo, ati Ambuye Yehova.

11. Ndipo kudzacitika tsiku ilo, ndidzapatsa Gogi manda m'Israyeli, cigwa ca opitawo kum'mawa kwa nyanja; ndipo lidzaletsa opitawo, ndipo adzaika komweko Gogi ndi unyinji wace wonse, nadzacicha, Cigwa ca unyinji wa Gogi.

12. Ndi a nyumba ya Israyeli adzapititsa miyezi isanu ndi iwiri alikuwaika, kuti ayeretse dziko.

13. Inde anthu onse a m'dziko adzawaika, nadzamveka nako tsiku lakulemekezedwa Ine, ati Ambuye Yehova.

14. Ndipo adzasankha anthu akupita-pitabe m'dziko, ndi pamodzi ndi opitapitawo anthu akuika mafupa otsala pamtunda, kuliyeretsa; pakutha miyezi isanu ndi iwiri adzapwaira.

15. Ndipo opitapitawo adzapitapita m'dziko, ndipo winaakaona pfupa la munthu aikepo cizindikilo, mpaka oikawo aliika m'cigwa ca unyinji wa Gogi.

Ezekieli 39