21. Koma ndinawaleka cifukwa ca dzina langa loyera, limene a nyumba ya Israyeli adalidetsa pakati pa amitundu, kumene adarakako,
22. Cifukwa cace nena kwa nyumba ya Israyeli, Atero Ambuye Yehova, Sindicicita ici cifukwa ca inu, nyumba ya Israyeli, koma cifukwa ca dzina langa loyera munaliipsalo pakati pa amitundu, kumene mudamukako.
23. Ndipo ndidzazindikiritsa dzina langa lalikuru kuti liri loyera, limene laipitsidwa mwa amitundu, limene inu munaliipsa pakati pao; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ati Ambuye Yehova, pozindikiridwa Ine woyera mwa inu pamaso pao.
24. Pakuti ndidzakutengani kukuturutsani kwa amitundu, ndi kukusokolotsani m'maiko onse, ndi kubwera nanu m'dziko lanu.