Eksodo 23:9-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Usampsinia mlendo; pakuti mudziwa mtima wa mlendo popeza munali alendo m'dziko la Aigupto.

10. Ndipo uzibzala m'munda mwako zaka zisanu ndi cimodzi, ndi kututa zipatso zako;

11. koma caka cacisanu ndi ciwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo ndipo zotsalira iwowa zoweta za kubusa zizidye; momwemo uzicita ndi munda wako wamphesa, ndimundawakowaazitona.

12. Uzicita nchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lacisanu ndi ciwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi buru wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakaziwako ndi mlendo atsitsimuke.

13. Ndipo samalirani zonse ndanena ndi inu; nimusachule dzina la milungu yina; lisamveke pakamwa pako.

14. Muzindicitira loe madyerero katatu m'caka.

15. Uzisunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda cotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unaturuka m'Aigupto; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu;

16. ndi madyerero a masika, zipatso zoyamba za nchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi madyerero a kututa, pakutha caka, pamene ututa nchito zako za m'munda.

Eksodo 23