Eksodo 14:27-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo Mose anatambasulira dzanja lace kunyanja, ndi nyanja inabwerera m'mayendedwe ace mbanda kuca; ndipo Aaigupto pothawa anakomana nayo; ndipo Yehova anakutumula Aaigupto m'kati mwa nyanja.

28. Popeza madziwo anabwerera, namiza magareta ndi apakavalo, ndiwo nkhondo yonse ya Farao imene idalowa pambuyo pao m'nyanja; sanatsala wa iwowa ndi mmodzi yense.

29. Koma ana a Israyeli anayenda pouma pakati pa nyanja; ndi madziwo anakhala ngati khoma kwa iwo, palamanja ndi palamanzere.

30. Comweco Yehova anapulumutsa Israyeli tsiku lomwelo m'manja a Aaigupto; ndipo Israyeli anaona Aaigupto akufa m'mphepete mwa nyanja.

Eksodo 14