4. Banja likaperewera mwana wa nkhosa, munthu ndi mnzace ali pafupi pa nyumba yace atenge monga mwa kufikira kwa anthu ao; muziwerengera mwana wa nkhosa monga mwa kudya kwao.
5. Mwana wa nkhosa wanu azikhala wangwiro, wamwamuna, wa caka cimodzi; muzimtenga ku nkhosa kapena ku mbuzi.
6. Ndipo mukhale naye cisungire kufikira tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi womwe; ndipo bungwe lonse la anthu a Israyeli lizimupha madzulo.
7. Ndipo azitengako mwazi, naupake pa mphuthu za mbali ndi ya pamwamba m'nyumba zimene adyeramo.
8. Ndipo azidya nyamayo usiku womwewo, yooca pamoto, ndi mkate wopanda cotupitsa; aidye ndi ndiwo zowawa,
9. Musaidya yaiwisi, kapena yophika ndi madzi konse ai, koma yooca pamoto; muti wace ndi miyendo yace ndi matumbo ace.
10. Ndipo musasiyako kufikira m'mawa; koma yotsalira kufikira m'mawayo muipsereze ndi moto: