Eksodo 11:7-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Koma palibe garu adzafunyitsira lilime lace ana onse a Israyeli ngakhale anthu kapena zoweta; kuti mudziwe kuti Yehova asiyanitsa pakati pa Aaigupto ndi Aisrayeli.

8. Ndipo anyamata ako onse awa adzanditsikira, nadzandigwadira, ndi kuti, Turukani inu, ndi anthu onse akukutsatani; ndipo pambuyo pace ndidzaturuka. Ndipo anaturuka kwa Farao wakupsa mtima.

9. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Farao sadzamvera inu; kuti zozizwa zanga zicuruke m'dziko la Aigupto.

10. Ndipo Mose ndi Aroni anacita zozizwa izi zonse pamaso pa Farao; koma Yehova analimbitsa mtima wace wa Farao, ndipo sanalola ana a Israyeli aturuke m'dziko lace.

Eksodo 11