Deuteronomo 6:10-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo kudzakhala, Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, kuti adzakupatsani ili; midzi yaikuru ndi yokoma, imene simunaimanga;

11. ndi nyumba zodzala nazo zokoma ziri zonse, zimene simunazidzaza, ndi zitsime zosema, zimene simunazisema, minda yampesa, ndi minda yaazitona, zimene simunazioka, ndipo mutakadya ndi kukhuta;

12. pamenepo mudzicenjere mungaiwale Yehova, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, m'nyumba ya akapolo,

13. Muziopa Yehova Mulungu wanu; ndi kutumikira Iyeyu; ndipo polumbira muzichula dzina lace.

14. Musamatsata milungu yina, milungu yina ya mitundu ya anthu akuzinga inu;

15. pakuti Yehova Mulungu wanu ali pakati panu, ndiye Mulungu wansanje; kuti ungapse mtima wa Yehova Mulungu wanu, ndi kukuonongani, kukucotsani pankhope pa dziko lapansi.

16. Musamayesa Yehova Mulungu wanu, monga munamyesa m'Masa.

Deuteronomo 6