1. Pamenepo tinatembenuka, ndi kubwera kumka njira ya ku Basana; ndipo Ogi mfumu ya Basana anaturuka kukomana nafe, kugwirana nafe nkhondo, iye ndi anthu ace onse, ku Edrei.
2. Ndipo Yehova anati kwa ine, Usamuopa; popeza ndampereka iye ndi anthu ace onse, ndi dziko lace, m'dzanja lako; umcitire monga umo unacitira Sihoni mfumu ya Aamori, amene anakhala m'Hesiboni.
3. Potero Yehova Mulungu wathu anaperekanso m'manja mwathu Ogi mfumu ya Basana, ndi anthu ace onse, ndipo tinamkantha kufikira sanamtsalira ndi mmodzi yense.