4. Ndipo kudzali, mutaoloka Yordano, muutse miyala iyi ndikuuzani lero, m'phiri la Ebala, ndi kuimata ndi njeresa.
5. Ndipo komweko mumangire Yehova Mulungu wanu guwa la nsembe, guwa la nsembe lamiyala; musakwezepo cipangizo cacitsulo.
6. Mumange guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu lamiyala yosasema; ndi kuperekapo nsembe zopsereza kwa Yehova Mulungu wanu;
7. ndi kuphera nsembe zoyamika, ndi kudyapo, ndi kukondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
8. Ndipo mulembere pa miyalayi mau onse a cilamulo ici mopenyeka bwino.
9. Ndipo Mose, ndi ansembe Alevi ananena ndi Israyeli wonse, ndi kuti, Khalani cete, imvanitu, Israyeli; lero lino mwasanduka mtundu wa anthu wa Yehova Mulungu wanu.
10. Potero muzimvera mau a Yehova Mulungu wanu, ndi kucita malamulo ace, ndi malemba ace, amene ndikuuzani lero lino.
11. Ndipo Mose anauza anthu tsiku lomwelo, ndi kuti,