1. Caka coyamba ca Belisazara mfumu ya ku Babulo Danieli anaona loto, naona masomphenya a m'mtima mwace pakama pace; ndipo analemba lotolo, nalifotokozera, mwacidule.
2. Danieli ananena, nati, Ndinaona m'masomphenya anga usiku, taonani, mphepo zinai za mumlengalenga zinabuka pa nyanja yaikuru.
3. Ndipo zinaturuka m'nyanja zirombo zazikuru zinai zosiyana-siyana.
4. Coyamba cinanga mkango, cinali nao mapiko a ciombankhanga, ndinapenyera mpaka nthenga zace zinathothoka, nicinakwezeka kudziko, ndi kuimitsidwa ndi mapazi awiri ngati munthu, nicinapatsidwa mtima wa munthu.
5. Ndipo taonani, cirombo cina caciwiri cikunga cimbalangondo cinatundumuka mbali imodzi; ndi m'kamwa mwace munali nthiti zitatu pakati pa mano ace; ndipo anatero naco, Nyamuka, lusira nyama zambiri.
6. Pambuyo pace ndinapenya ndi kuona cina ngati nyalugwe, cinali nao mapiko anai a nkhuku pamsana pace, ciromboco cinali nayonso mitu inai, nicinapatsidwa ulamuliro.
7. Pambuyo pace ndinaona m'masomphenya a usiku, ndi kuona cirombo cacinai, coopsa ndi cocititsa mantha, ndi camphamvu coposa, cinali nao mano akuru acitsulo, cinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza cotsala ndi mapazi ace; cinasiyana ndi zirombo zonse zidacitsogolera; ndipo cinali ndi nyanga khumi.