Danieli 3:17-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Taonani, Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m'ng'anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m'dzanja lanu, mfumu.

18. Koma akapanda kutero, dziwani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolidi mudaliimikalo.

19. Pamenepo Nebukadinezara anadzazidwa ndi ukali, ndi maonekedwe a nkhope yace anasandulikira Sadrake, Mesake, ndi Abedinego; anayankha, nati asonkheze ng'anjo kasanu ndi kawiri koposa umo amasonkhezera.

20. Nauza amuna ena amphamvu a m'khamu lace la nkhondo amange Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, ndi kuwaponya m'ng'anjo yotentha yamoto.

21. Pamenepo amuna awa anamangidwa ali cibvalire zopfunda zao, maraya ao, ndi nduwira zao, ndi zobvala zao zina; naponyedwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.

22. Motero, popeza mau a mfumu anafulumiza, ndi ng'anjo inatentha koposa, lawi la moto linapha iwo aja ananyamula Sadrake, Mesake, ndi Abedinego.

23. Ndipo amuna atatu awa, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, anagwa pansi omangidwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.

Danieli 3