1. Mfumu Nebukadinezara anapanga fano lagolidi, msinkhu wace mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi thunthu lace mikono isanu ndi umodzi; analiimika pa cidikha ca Dura, m'dera la ku Babulo.
2. Ndipo mfumu Nebukadinezara inatumiza kukasonkhanitsa akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga cuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, abwere kuzurula fanoli adaliimika mfumu Nebukadinezara.
3. Pamenepo akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga cuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, anasonkhanira kupereka fano adaliimika mfumu Nebukadinezara, naimirira pamaso pa fano adaliimika Nebukadinezara.
4. Ndipo wolalikira anapfuulitsa, kuti, Akulamulirani inu anthu, mitundu ya anthu a manenedwe osiyana,
5. kuti pakumva inu mau a lipenga, citoliro, zeze, sansi, cisakasa, ngoli, ndi zoyimbitsa ziri zonse, mugwadire ndi kulambira fano lagolidi adaliimika mfumu Nebukadinezara;
6. ndipo ali yense wosagwadira ndi kulambira, adzaponyedwa nthawi yomweyo m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.
7. Potero nthawi yomweyo pakumva anthu onse mau a lipenga, citoliro, zeze, sansi, cisakasa, ndi zoyimbitsa ziri zonse, anthu onse, mitundu ya anthu a manenedwe osiyana, anagwadira, nalambira fano lagolidi adaliimika mfumu Nebukadinezara.
8. Cifukwa cace anayandikira Akasidi ena nthawi yomweyi, naneneza Ayuda.
9. Anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Mfumu, mukhale ndi moyo cikhalire.