5. Pamenepo ine Danieli ndinapenya, ndipo taonani, anaimapo awiri ena, wina m'mphepete mwa mtsinje tsidya lino, ndi mnzace m'mphepete mwa mtsinje tsidya lija.
6. Ndipo wina anati kwa munthu wobvala bafuta, wokhala pamwamba pa madzi a mumtsinje, Cimariziro ca zodabwiza izi cidzafika liti?
7. Ndipo ndinamva munthuyo wobvala bafuta wokhala pamwamba pa madzi a mumtsinje, nakweza dzanja lace lamanja ndi lamanzere kumwamba, nalumbira pali Iye wokhala ndi moyo kosatha, kuti zidzacitika nthawi, ndi nthawi zina, ndi nusu; ndipo atatha kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo zidzatha izi zonse.
8. Ndinacimva ici, koma osacizindikira; pamenepo ndinati Mbuye wanga, citsiriziro ca izi nciani?
9. Ndipo anati, Pita Danieli; pakuti mauwo atsekedwa, nakomeredwa cizindikilo mpaka nthawi ya citsiriziro.
10. Ambiri adzadzitsuka ndi kudziyeretsa, nadzayesedwa ndi moto; koma oipa adzacita moipa; ndipo palibe mmodzi wa oipa adzazindikira; koma aphunzitsi ndiwo adzazindikira.