20. Pamenepo anati, Kodi udziwa cifukwa coti ndakudzera? ndipo tsopano ndibwerera kulimbana ndi kalonga wa Perisiya; ndipo pomuka ine, taonani, adzadza kalonga wa Helene.
21. Koma ndidzakufotokozera colembedwa pa lemba la coonadi; ndipo palibe wina wakudzilimbikitsa pamodzi ndi ine, kutsutsana ndi aja, koma Mikaeli kalonga wanu.