1. Zitatha izi ndinaona mngelo wina wakutsika m'Mwamba wakukhala nao ulamuliro waukuru; ndipo dziko linaunikidwa ndi ulemerero wace.
2. Ndipo anapfuula ndi mau olimba, nanena, Wagwa, wagwa, Babulo waukuru, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa.
3. Cifukwa ndi vinyo wa mkwiyo wa cigololo cace mitundu yonse idagwa; ndipo mafumu a dziko anacita naye cigololo; ndipo ocita malonda a dziko analemera ndi mphamvu ya kudyererakwace.
4. Ndipo ndinamva mau ena ocokera Kumwamba, nanena, Turukani m'menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi macimo ace, ndi kuti mungalandireko ya miliri yace;
5. pakuti macimo ace anaunjikizana kufikira m'Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zace.
6. Muubwezere, monganso uwu unabwezera, ndipo muwirikize kawiri, monga mwa nchito zace; m'cikhomo unathiramo, muuthirire cowirikiza.