Cibvumbulutso 16:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo waciwiri anatsanulira mbale yace m'nyanja; ndipo kunakhala mwazi ngati wa munthu wakufa; ndipo zamoyo zonse za m'nyanja zidafa.

4. Ndipo wacitatu anatsanulira mbale yace ku mitsinje ndi akasupe a madzi; ndipo kunasanduka mwazi.

5. Ndipo ndinamva mngelo wa madziwo nanena, Muli wolungama, amene muli, nimunali, Woyera Inu, cifukwa mudaweruza kotero;

6. popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo.

7. Ndipo ndinamva wa pa guwa la nsembe, alinkunena, Inde, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, maweruziro anu ali oona ndi olungama.

8. Ndipo wacinai anatsanulira mbale yace padzuwa; ndipo analipatsa ilo litenthe anthu ndi moto.

Cibvumbulutso 16