Cibvumbulutso 16:2-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo anacoka woyamba, natsanulira mbale yace kudziko; ndipo kunakhala cironda coipa ndi cosautsa pa anthu akukhala nalo lemba la cirombo nalambira fano lace.

3. Ndipo waciwiri anatsanulira mbale yace m'nyanja; ndipo kunakhala mwazi ngati wa munthu wakufa; ndipo zamoyo zonse za m'nyanja zidafa.

4. Ndipo wacitatu anatsanulira mbale yace ku mitsinje ndi akasupe a madzi; ndipo kunasanduka mwazi.

5. Ndipo ndinamva mngelo wa madziwo nanena, Muli wolungama, amene muli, nimunali, Woyera Inu, cifukwa mudaweruza kotero;

6. popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo.

7. Ndipo ndinamva wa pa guwa la nsembe, alinkunena, Inde, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, maweruziro anu ali oona ndi olungama.

Cibvumbulutso 16