Cibvumbulutso 16:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ndinamva mau akuru ocokera kuKacisi, akunena kwa angelo asanu ndi awiri, Mukani, ndipo tsanulirani kudziko mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu.

2. Ndipo anacoka woyamba, natsanulira mbale yace kudziko; ndipo kunakhala cironda coipa ndi cosautsa pa anthu akukhala nalo lemba la cirombo nalambira fano lace.

3. Ndipo waciwiri anatsanulira mbale yace m'nyanja; ndipo kunakhala mwazi ngati wa munthu wakufa; ndipo zamoyo zonse za m'nyanja zidafa.

Cibvumbulutso 16