Aroma 8:32-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. iye amene sanatimana Mwana wace wa iye yekha, koma 7 anampereka cifukwa ca ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi iye?

33. Ndani adzaneneza osankhidwa a Mulungu? 8 Mulungu ndiye ameneawayesa olungama;

34. 9 ndani adzawatsutsa? Kristu Yesu ndiye amene adafera, inde makamaka, ndiye amene adauka kwa akufa, 10 amene akhalanso pa dzanja lamanja la Mulungu, 11 amenenso atipempherera ife.

35. Adzatisiyanitsa ndani ndi cikondi ca Kristu? nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsya kapena lupanga kodi?

36. Monganso kwalembedwa,12 Cifukwa ca Inu tirikuphedwa dzuwa lonse;Tinayesedwa monga nkhosa zakupha,

37. Koma 13 m'zonsezi, ife tilakatu, mwa iye amene anatikonda.

Aroma 8