Aroma 11:6-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Koma ngati kuli ndi cisomo, sikulinso ndinchito ai; ndipo pakapanda kutero, cisomo sicikhalanso cisomo.

7. Ndipo ciani tsono? ici cimene Israyeli afunafuna sanacipeza; koma osankhidwawo anacipeza, ndipo otsalawo anaumitsidwa mtima;

8. monga kunalembedwa kuti, Mulungu anawapatsa mzimu watulo, maso kuti asapenye, ndi makutu kuti asamve, kufikira lero lino.

9. Ndipo Davide akuti,Gome lao likhale kwa iwo, ngati msampha, ndi ngati diwa,Ndi monga cokhumudwitsa, ndi cowabwezera cilango;

10. Maso ao adetsedwe, kuti asapenye,Ndipo muweramitse msana wao masiku onse.

11. Cifukwa cace ndinena, Anakhumudwa kodi kuti agwe? Msatero ai; koma ndi kulakwa kwao cipulumutso cinadza kwa anthu akunja, kudzacititsa iwo nsanje.

12. Ndipo ngati kulakwa kwao kwatengera dzikolapansi zolemera, ndipo kucepa kwao klltengera anthu amitundu zolemera; koposa kotani nanga kudzaza kwao?

13. Koma ndilankhula ndi inu anthu amitundu. Popeza ine ndiri mtumwi wa anthu amitundu, millemekeza utumiki wanga;

14. kuti ngati nkutheka ndikacititse nsanje amenewo a mtundu wanga; ndi kupulumutsa ena a iwo.

Aroma 11