3. Ndipo ici tidzacita, akatilola Mulungu.
4. Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yace, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera,
5. nalawa mau okoma a Mulungu, ndi mphamvu ya nthawi irinkudza,
6. koma anagwa m'cisokero; popeza adzipaeikiranso okha Mwana wa Mulungu, namcititsa manyazi poyera.
7. Pakuti nthaka imene idamwa mvula iigwera kawiri kawiri, nipatsa therere loyenera iwo amene adailimira, ilandira dalitso locokera kwa Mulungu:
8. koma ikabala minga ndi mitungwi, itayika; nitsala pang'ono ikadatembereredwa; citsiriziro cace ndico kutenthedwa.
9. Koma, okondedwa, takopeka mtima kuti za inu ziri zoposa ndi zophatikana cipulumutso, tingakhale titero pakulankhula;
10. pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala nchito yanu, ndi cikondico mudacionetsera ku dzina lace, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.