1. Cifukwa cace tiope kuti kapena likatsala lonjezano lakulowa mpumulo wace, wina wa inu angaoneke ngati adaliperewera.
2. Pakuti kwa ifenso walalikidwa Uthenga Wabwino, monganso kwa iwo; koma iwowa sanapindula nao mau omvekawo, popeza sanasanganizika ndi cikhulupiriro mwa iwo amene adawamva.
3. Popeza ife amene takhulupira tilowa mpumulowo, monga momwe ananena,Monga ndalumbira mu mkwiyowanga,Ngati adzalowa mpumulo wanga:zingakhale nebitozo zidatsirizika kuyambira kuzika kwa dziko lapansi.