4. Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.
5. Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi.
6. Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.
7. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana cidziwitso conse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.
8. Cotsalira, abale, zinthu ziri zonse zoona, ziri zonse zolemekezeka, ziri zonse zolungama, ziri zonse zoyera, ziri zonse zokongola, ziri zonse zimveka zokoma; ngati kuli cokoma mtima cina, kapena citamando cina, zilingirireni izi.
9. Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo citani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.
10. Koma ndinakondwera mwa Ambuye kwakukuru, kuti tsopano munatsitsimukanso kulingirira mtima za kwa ine, kumenekonso munalingirirako, koma munasowa pocitapo.