2 Samueli 17:23-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndipo Ahitofeli, pakuona kuti sautsata uphungu wace anamanga buru wace, nanyamuka, nanka kumudzi kwao, nakonza za pa banja lace, nadzipacika, nafa, naikidwa m'manda a atate wace.

24. Ndipo Davide anafika ku Mahanaimu. Abisalomu naoloka Yordano, iye ndi anthu onse a Israyeli pamodzi naye.

25. Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yoabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lace Itra M-israyeli, amene analowa kwa Abigayeli, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yoabu.

26. Ndipo Israyeli ndi Abisalomu anamanga zithando m'dziko la Gileadi.

2 Samueli 17