22. Pomwepo Davide ananyamuka ndi anthu onse amene anali naye, naoloka Yordano. Kutaca m'mawa sanasowa mmodzi wa iwo wosaoloka Yordano.
23. Ndipo Ahitofeli, pakuona kuti sautsata uphungu wace anamanga buru wace, nanyamuka, nanka kumudzi kwao, nakonza za pa banja lace, nadzipacika, nafa, naikidwa m'manda a atate wace.
24. Ndipo Davide anafika ku Mahanaimu. Abisalomu naoloka Yordano, iye ndi anthu onse a Israyeli pamodzi naye.
25. Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yoabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lace Itra M-israyeli, amene analowa kwa Abigayeli, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yoabu.