13. Ndikatseka kumwamba kuti pasakhale mvula, kapena ndikalamulira dzombe lithe za padziko, kapena ndikatumiza mliri mwa anthu anga;
14. ndipo anthu anga ochedwa dzina langa akadzicepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zao zoipa; pamenepo ndidzamvera m'Mwamba, ndi kukhululukira coipa cao, ndi kuciritsa dziko lao.
15. Tsopano maso anga adzakhala otsegukira, ndi makutu anga ochera, pemphero la m'malo ano.
16. Pakuti ndasankha ndi kuipatula nyumba Iyi, kuti dzina langa likhaleko cikhalire; inde maso anga ndi mtima wanga zidzakhala komweko kosalekeza.
17. Ndipo iwe ukadzayenda pamaso panga monga umo anayendera Davide atate wako, nukacita monga mwa zonse ndakulamulira iwe, nukasunga malemba anga ndi maweruzo anga;
18. pamenepo ndidzakhazikitsa mpando wacifumu wa ufumu wako, monga ndinapangana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wokhala mfumu m'Israyeli.