10. Ndipo tsiku la makumi awiri ndi citatu la mwezi wacisanu ndi ciwiri anawauza anthu apite ku mahema ao, akusekera ndi kukondwera m'mtima mwao cifukwa ca zokoma Yehova adawacitira Davide, ndi Solomo, ndi Aisrayeli anthu ace.
11. Momwemo Solomo anatsiriza nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu; ndipo ziri zonse zidalowa mumtima mwace mwa Solomo kuzicita m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba yace yace, anacita mosabwezeza.
12. Ndipo Yehova anaonekera kwa Solomo usiku, nanena naye, Ndamva pemphero lako, ndadzisankhira malo ano akhale nyumba ya nsembe.
13. Ndikatseka kumwamba kuti pasakhale mvula, kapena ndikalamulira dzombe lithe za padziko, kapena ndikatumiza mliri mwa anthu anga;
14. ndipo anthu anga ochedwa dzina langa akadzicepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zao zoipa; pamenepo ndidzamvera m'Mwamba, ndi kukhululukira coipa cao, ndi kuciritsa dziko lao.