2 Mbiri 28:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi; koma sanacita zoongoka pamaso pa Yehova ngati Davide kholo lace,

2. koma anayenda m'njira za mafumu a Israyeli, napangiranso Abaala mafano oyenga,

3. Nafukizanso yekha m'cigwa ca mwana wa Hinomu, napsereza ana ace m'moto, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawainga pamaso pa ana a Israyeli.

4. Naphera nsembe, nafukiza kumisanje, ndi kuzitunda, ndi patsinde pa mtengo uli wonse wogudira.

5. Cifukwa cace Yehova Mulungu wace anampereka m'dzanja la mfumu ya Aramu; ndipo anamkantha, natenga ndende unyinji waukuru wa anthu ace, nafika nao ku Damasiko. Anaperekedwanso iye m'dzanja la mfumu ya Israyeli, amene anamkantha makanthidwe akuru.

2 Mbiri 28