2 Mbiri 23:2-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo iwo anayendayenda mwa Yuda, nasonkhanitsa Alevi m'midzi yonse ya Yuda, ndi akuru a nyumba za makolo m'Israyeli; nadza iwo ku Yerusalemu.

3. Ndipo msonkhano wonse unapangana pangano ndi mfumu m'nyumba ya Mulungu. Ndipo ananena nao, Taonani, mwana wa mfumu adzakhala mfumu monga Yehova ananena za ana a Davide.

4. Cimene muzicita ndi ici: limodzi la magawo atatu mwa inu olowera dzuwa la Sabata, la ansembe ndi Alevi, akhale olindirira pakhomo;

2 Mbiri 23