9. Ndipo anaphunzitsa m'Yuda ali nalo buku la cilamulo la Yehova, nayendayenda m'midzi yonse ya Yuda, naphunzitsa mwa anthu.
10. Ndipo kuopsa kwa Yehova kunagwera maufumu a maiko ozungulira Yuda; momwemo sanayambana ndi Yehosafati.
11. Ndipo Afilisti ena anabweca nazo kwa Yehosafati mitulo, ndi ndalama za msonkho; Aarabu omwe anabwera nazo kwa iye zoweta, nkhosa zamphongo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri ndi atonde zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri.
12. Ndipo Yehosafati anakula cikulire, namanga m'Yuda nyumba zansanja, ndi midzi ya cuma.