7. Ndipo ananena naye, kuti, Mukawacitira cokoma anthu awa, ndi kuwakonda, ndi kulankhula nao mau okoma, adzakhala anyamata anu kosatha.
8. Koma analeka uphungu wa akulu akuluwa adampangirawo, nakafunsana ndi anyamata anakula naye pamodzi, oimirira pamaso pace.
9. Nati nao, Mundipangire bwanji inu, kuti tibwezere mau anthu awa ananena nanewo, ndi kuti, Mupepuze goli limene atate wanu anatisenzetsa ife?
10. Ndipo anyamatawo adakula naye pamodzi ananena naye, ndi kuti, Muzitero nao anthu awa adalankhula nanu, ndi kuti, Atate wanu analemeretsa goli lathu, koma inu mutipepuzire ilo; muzitero nao, Kanense wanga adzaposa m'cuuno mwa atate wanga.
11. Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzetsani goli lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.
12. Tsono Yerobiamu ndi anthu onse anabwera kwa Rehabiamu tsiku lacitatu, monga mfumu idanena, ndi kuti, Bweraninso kwa ine tsiku lacitatu.
13. Ndipo mfumu inawayankha mokaripa, popeza mfumu Rehabiamu analeka uphungu wa akulu akulu,
14. nalankhula nao monga umo anampangira acinyamata, ndi kuti, Atate wanga analemeretsa goli lanu, koma ine ndidzaonjezerapo; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.
15. Momwemo mfumu siinamvera anthuwo; pakuti kusinthaku kudafuma kwa Mulungu, kuti Yehova akhazikitse mau ace, amene ananenetsa Ahiya wa ku Silo kwa Yerobiamu mwana wa Nebati.