2 Mbiri 1:2-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo Solomo analankhula ndi Aisrayeli onse, ndi akuru a zikwi ndi a mazana, ndi kwa oweruza, ndi kwa kalonga ali yense wa Israyeli, akuru a nyumba za makolo.

3. Ndipo Solomo ndi khamu lonse pamodzi naye anamuka ku msanje wa ku Gibeoni; pakuti kumeneko kunali cihema cokomanako ca Mulungu adacimanga Mose mtumiki wa Yehova m'cipululu.

4. Koma likasa la Mulungu Davide adakwera nalo kucokera ku Kiriyati Yearimu kumka kumene Davide adalikonzeratu malo; pakuti adaliutsiratu hema ku Yerusalemu.

2 Mbiri 1