37. Iye nalowa, nagwa pa mapazi ace, nadziweramitsa pansi; nanyamula mwana wace, naturuka.
38. Ndipo Elisa anabwera ku Giligala, koma m'dzikomo munali njala; ndi ana a aneneri anali kukhala pansi pamaso pace; ndipo anati kwa mnyamata wace, Ika nkhali yaikuruyo, uphikire ana a aneneri.
39. Naturuka wina kukachera ndiwo kuthengo, napeza conga ngati mpesa, nacherapo zipuzi kudzaza m'pfunga mwace, nadza, nazicekera-cekera m'nkhali ya cakudya, popeza sanazidziwa.
40. Pamenepo anagawira anthu kuti adye. Koma kunali; pakudya cakudyaco, anapfuula nati, Munthu wa Mulungu, muli imfa m'nkhalimo. Ndipo sanatha kudyako.
41. Pamenepo anati, Bwera naoni ufa. Nathira m'nkhalimo; nati, Gawirani anthu kuti adye. Ndipo m'nkhalimo munalibe cowawa.