2 Mafumu 2:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pamenepo ana a aneneri okhala ku Yeriko anayandikira kwa Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akucotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati iye, Inde ndidziwa, khalani muli cete.

6. Ndipo Eliya ananena naye, Ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yordano, Nati iye, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Napitirira iwo awiri.

7. Ndipo anthu makumi asanu a ana a aneneri anapita, naima patali pandunji pao, iwo awiri naima ku Yordano.

8. Ndipo Eliya anagwira copfunda cace, nacipindapinda napanda madzi, nagawikana kwina ndi kwina; ndipo anaoloka iwo onse awiri pansi pouma.

9. Ndipo kunali ataoloka, Eliya anati kwa Elisa, Tapempha cimene ndikucitire ndisanacotsedwe kwa iwe. Ndipo Elisa anati, Mundipatse magawo awiri a mzimu wanu akhale pa ine.

10. Nati iye, Wapempha cinthu capatali, koma ukandipenya pamene ndicotsedwa kwa iwe, kudzatero nawe; koma ukapanda kundipenyapo, sikudzatero at.

2 Mafumu 2