1. Caka cakhumi ndi ziwiri ca Ahazi mfumu ya Yuda Hoseya mwana wa Ela analowa ufumu wace wa Israyeli m'Samariya, nakhala mfumu zaka zisanu ndi zinai.
2. Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, koma osati monga mafumu a Israyeli asanakhale iye.
3. Anamkwerera Salimanezere mfumu ya Asuri kumthira nkhondo; ndipo Hoseya anamgonjera, namsonkhera mitulo.