2 Mafumu 16:18-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Nacotsa ku nyumba ya Yehova malo ophimbika a pa Sabata adawamanga kunyumba, ndi polowera mfumu pofuma kunja, cifukwa ca mfumu ya Asuri.

19. Macitidwe ena tsono adawacita Ahazi, salembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

20. Nagona Ahazi ndi makolo ace, namuika ndi makolo ace m'mudzi wa Davide; nakhala mfumu m'malo mwace Hezekiya mwana wace.

2 Mafumu 16